Chipani cha Democratic Progressive (DPP) chati chili ndi chiyembekezo chodzatenganso boma pa chisankho chapatatu chomwe chikubwera chaka chamawa.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi m’chigawo chakum’mawa Bright Msaka wanena izi pa msonkhano wa ndale womwe unachitikira ku wadi ya Mwasa m’boma la Mangochi.
Msaka adati boma lomwe lilipoli lalephera ndipo adanenetsa kuti DPP ndi chipani chokhacho chomwe chimasamala za umoyo wa anthu.
Iye walimbikitsa anthu kidelari kuti avotere khansala wa DPP...