Chipani chotsutsa boma cha Peoples Development (PDP) chati chidzatenga nowo gawo pa chisankho cha 2025, poyima paokha.
Mtsogoleri wa chipanichi a Kondwani Nankhumwa anena izi pa msonkhano waukulu wa chipanichi ku Blantyre.
M’mawu awo ati anthu ena akhala akuganiza kuti chipani cha PDP chilibe chikoka kumadera a mdziko muno koma lero azionela okha.
Iwo ati kudzera pa msonkhanowu pomwe pabwera nthumwi zochokera maboma onse mdziko lino, ndichitsimikizo kuti chipanichi...